Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 219

Matigari Musalole kuti mantha akusungunuleni, ndipo onse abalalike ndi kulira kosalekeza kwa mfuti yanu." Matigari anawerama ngati mtolo wa udzu ndipo kenako anayang'ana kumbali. Iye anayamba kumva kutentha kwa misozi yomwe inalengeza m'maso mwake. "Tiyeni tiuyambe!" Matigari ananena mokhala ngati akufuna kulira komanso movutikira kwambiri. "Tsopano tiziyendera mfundo yakuti, Cho m we tanena tanena, tiyeni tichichite!" Koma mwadzidzidzi anangomva kulira kwa galimoto. Nthawi yomweyo anayamba kuyang'anizana. Galimoto ikupezeka bwanji kutchire kuno? Ikudzataniko kuno? 218