Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 210
Matigari
*Nyinyi wenda wazimu (Kiswahili): Kutanthauza kuti " ndinu anthu osokonekera mitu,
amisala."
Gawo 8
. . . Ino ndi Wailesi Yanu ya Choonadi . . . tsopano mvetserani
chidziwitso china chapadera . . . Nduna Yoona Zachilungamo
yalamula apolisi kuti awombere amisala onse omwe angakumane nawo
akungoyendayenda m’misewu . . .
Gawo 9
Apolisi aika malo ochitira chipikisheni m'misewu yonse ya m'dzi-
ko muno pamene akupitiriza kufufuza amisala omwe athawa ku-
chipatala. Galimoto zambiri, makamaka mabasi komanso matatu, ziku-
machitidwa chipikisheni zisanadutse. Zikuoneka kuti amisala ena
akhoza kukwera mabasi komanso magalimotowa kuti athawe. Apolisi
akupempha oyendetsa mabasi komanso matatu ndiponso
owathandizira awo kuti anene kupolisi ngati munthu wina wanena
kuti alibe ndalama yoti alipirire basi chifukwa zikuoneka kuti amisala-
wa alibe ndalama iliyonse. Ena onse amene akuyenda pansewu aku-
pemphedwa kuti anene kupolisi akaona munthu aliyense akuimitsa
galimoto . . .
209