Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 202
Matigari
Gawo 18
Atangopititsidwa kuchipatala cha amisala chija, Matigari ma
Njiruungi ndi Ngaruro wa Kiriro anakambirana usiku wonse zo-
khudza ogwira ntchito aja . . . alimi . . . omenyera ufulu wa an-
thu . . . oukira boma . . . komanso nkhani zonse zokhudza ku-
menya nkhondo kuti ana a m’tsogolo adzakhale pabwino . . .
Ankangokhala ngati mphunzitsi ndi wophunzira wake.
Nthawi ina mphunzitsi ankakhala Matigari, koma kenako zin-
kasintha n'kukhalanso Ngaruro.
Kenako mbalame zinayamba kuimba:
Kunjaku kukanachaa,
Kunjaku kukanachaa,
n'kadapita kukasamba madzi ozizira limodzi ndi mbalame zam'mawa.
Guthera ndi Muriuki anabwerera kwawo, koma aliyense
ankadzifunsa atagona pakama wake kuti: Kod i nd ingachite
chiyani kuti ndithandize . . . ?
201