Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 200
Matigari
Anthu aja anapitirizabe kuimba mosaleletseka. Posakhalitsa
apolisi anayambanso kuliza mizinga.
"Msonkhanowu wathera pamenepa!" nduna ija inatero.
"Zipitani m'makwanu! Nonse mukhoza kumapita m'makwanu
tsopano!"
"Pasapezeke munthu woima penapake! Komanso simukulo-
ledwa kumayenda m'magulu a anthu oposa asanu," wapolisi uja
anawonjezera.
Koma pa nthawiyi n'kuti anthu aja akuimba mokweza
kwambiri kuposa poyamba paja. Ena anayamba kukuwa kuti
akufuna kuti Ngaruro wa Kiriro amasulidwe. Ena ankanena
mawu akuti, "Atuluke m'boma anthu onse akuba komanso
abodza!"
"Ndaletsanso kuti anthu asamapezeke ali m'magulu m'mi-
dzimu," bwanamkubwa uja anatero. "Ndalamula mafumu onse
kuti agwiritsire ntchito mphamvu zomwe anapatsidwa ndi
lamulo la Chiefs Act. Ndikuwapatsa mphamvu zoti akhoza ku-
manga munthu aliyense amene apezeke akuyendayenda
m'mudzi popanda sababu.*"
*Sababu (Kiswahili): Kutanthauza popanda chifukwa.
Anthu aja anaimirira n'kuyamba kuimba molowera komwe
kunali ndunayo akuimba ngati akunena kuti akufuna kupita ku-
chipinda anatsekera Matigari ma Njiruungi, Ngaruro wa Kiriro
komanso anthu ena anapalamula milandu yokhudzana ndi
ndale aja kuti akawatulutse.
Mkulu wa apolisi uja analiza wizilo. Nthawi yomweyo apoli-
si komanso asilikali aja anayamba kuthamangitsa anthu aja
n'kumawamenya ndi matabwa a mfuti zawo. Anthu anayamba
199