Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 193
Matigari
malamulo a m'dziko muno. Choncho ndine wokonzeka kugwiri-
zana ndi chigamulo chimene oweruza athu apanga, chifukwa
nanenso ndili pansi palamulo, ndipo ndimakhulupirira kuti
oweruza milandu ayenera k uk hala m bali yoim a payo k ha.
Chabwino, tsopano mvetserani chigamulo chimene
chaperekedwa mosamala kwambiri."
"Wophunzira komanso mphunzitsi ayenera kutsekeredwa
m'ndende kuti aimbidwe mlandu wopezeka ndi zinthu zoletsed-
wa. Makhoti sangalole kuti anthu ophunzira asokoneze anthu a
m'dziko muno ndi ziphunzitso za Marx komanso ziphunzitso zi-
na za chikomyunizimu."
Wophunzira uja anamangidwa ndi unyolo limodzi ndi
mphunzitsi uja. Zimenezi zinamuwawa mumtima koopsa ndipo
analimba mtima ngati mkango n'kuyamba kuyankhula. Anali
asanayambe wachitapo zangati zimenezi pamoyo wake. Anaku-
wa kuti:
"Muzikumbukira nthawi zonse zimene Matigari wakuuzani
zija. Chiwanda chakuba sichikhutira ndi nsembe zimene anthu
amachipatsa. Tsopano ndasukusula ndipo ndikutha kuona zime-
nezi bwinobwino ngakhale m'chipinda muno. Ndipitirizabe
kuimba mogwirizana ndi anzanga omwe anamangidwa dzulo
komanso dzana, ndiponso ophunzira makumi asanu omwe
aphedwa m'mawa walero ndi apolisi:
Ngakhale mutitsekere m'ndende,
Chipambano ndi chathu!
Chipambano ndi chathu!
Aliyense anangokhala chete. Tsopano anazindikira kuti
mphekesera zoti ophunzira makumi asanu aphedwa zija ndi zo-
ona.
192