Matigari
ntchito. Karl Marx ameneyu akusokoneza ophunzira, aphunzitsi
komanso ogwira ntchito athu. Mabuku komanso zinthu za
anthu amenewa ziyenera kuletsedwa kotheratu m’dziko muno.
Ndikunena kuti mabuku komanso zinthu zina za Karl Marx,
Lenin komanso Mao zisadzapezekenso m’dziko lathu lino.”
Kenako anaimba mavesi awiri m’buku la Songs o f a Parro t
n’kukhala pansi.
Tsopano phungu wa kunyumba yamalamulo anaimirira. Iye
anavala suti yoterela, taye yokhala ndi zilembo zija za KKK
komanso magalasi a dzuwa aakulu mosagwirizana ndi mutu
wake. Asanayambe kuyankhula anaimba kaye mavesi awiri
m’buku lija la So ngs o f a Parro t. Kenako anayamba kuyankhula.
“Ndikufuna kuphera mphongo zimene anzanga anena kale.
Koma ndikufunanso kuwonjezera mfundo imodzi. Mfundo yake
ndi yonena za Matigari ma Njiruungi. Ndamva zoti azimayi ena
akumanena zoti abereka a Matigari ma Njiruungi ambiri. Kodi
mwazerezeka naye kale Matigari ma Njiruungiyu? Boma la KKK
lakhala likunena kuti gwero la umphawi womwe uli m’dziko
muno ndi loti azimayi akumabereka ana ngati makoswe!
Ngakhale m’nthawi ya atsamunda pamene ndinkagwira ntchito
m’dipatimenti ya Co m m unity and Social Welfare, ankatiuza kuti
kukhala ndi ana ambiri si kwabwino. Anthu ayenera kumakhala
ndi ana mogwirizana ndi mmene m’thumba mwawo mulili.
Amene alibe ndalama asamadzivutitse n’kumabereka ana.
Ndipempha boma la USA kuti litsegule chipatala chaulere kuti
azimayi azikatseketsa kumeneko. Anthu osauka ayenera kusiya
kubereka ana! Ayenera kusiyira udindo umenewu anthu
olemera. Mwaona, zikanakhala kuti anthu sakubereka ana
ambirimbiri, sipakanakhala mikangano ya pakati pa ogwira
ntchito ndi owalemba ntchito pankhani ya malipiro.
189