Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 183

Matigari ufulu wa dziko lathu abweranso kuti adzatenge zinthu zawo!’ Mkulu wa apolisi uja ankayang’anabe Matigari mwachidwi kwambiri. Maso ake anangoti ga pamanja a Matigari. Mwapang’onopang’ono komanso mochenjera kwambiri, anapititsa dzanja lake m’chiuno. Kenako mosaonetsera anayamba kumasula kachikwama komwe anaikamo mfuti yake. Nduna ija inati, “Oh . . . Ndiwe Matigari ma Njiruungi! Bwera kutsogolo kuno! Bwera kuti tikuone bwinobwino.” Apolisi ena anayamba kutsatira pang’onopang’ono Matigari. Koma Matigari anawaopseza ponena kuti, “Musayerekeza kundigwira! Ndiyenda ndekha, mapazi ndili nawo.” Anthu omwe anakhala mopanikizana m’holoyo anayamba kufutuka n’kumapereka njira kwa Matigari. Alendo onse anali kutsogolo aja analinso ndi maganizo ofanana ndi omwe mkulu wa apolisi uja anali nawo, oti Matigari ali ndi mfuti. Onse anangoti maso ga pamanja a Matigari. Milomo ya wansembe uja inayamba kugwedezeka ndipo zikuoneka kuti ankapereka pemphero lachinunu. Pamene Matigari ankayandikira kutsogolo, mkulu wa apolisi uja anasolola mofulumira mfuti yake kuchoka m’kachikwama kaja ndipo anamulozetsa Matigari, akukuwa kuti, “Manja m’mwamba!” Matigari anachotsa manja ake aja m’matumba akumwetulira, ndipo anazindikira chifukwa chake mkulu wa apolisiyo anali ndi mantha osaneneka. Kenako ananena kuti, “Musandiope, ine ndadzimanga ndi lamba wamtendere.” Koma mkulu wa apolisiyo anali asanakhutirebe kuti Matigari alibe mfuti. Kenako anapereka chizindikiro kwa apolisi awiri kuti akamuseche. 182