Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 177
Matigari
ena n’kukamutsekera kundende. Palibe boma limene
linganyengerere munthu wovutitsa komanso kulola kuti
munthu m’modzi aphwanye maufulu a anthu mamiliyoni
ambirimbiri omwe ali m’dziko muno. Ndi ndani amene
angalolere kutaya thumba lathunthu lachimanga chifukwa choti
chimanga chimodzi n’chowola? Amangochotsa kachimanga
kowolako n’kukataya. Eetu! Nacho nso chim anga cho tsalacho
chili ndi ufulu wawo!”
“Ndiye musatichititse manyazi pamaso pa alendowa.
Tamafunsani mafunso. Sitikufuna kuti wina akawotche
gombeza! Ndikubwerezanso, pali wina amene ali ndi funso?”
“Inde!” Munthu wina anatero.
Maso a anthu onse anali m’chipindacho anatembenukira kwa
munthuyo yemwe anali chakukhomo kwenikweni kwa holoyo.
Munthu wamtali, wathupi lodzinga komanso wooneka
wachikulire, anaima chapakhomo. Pamutu pake panali chipewa
chakhonde, chomwe anachimanga ndi chingwe pachigama pake.
Chipewacho chinali chokongoletsedwa mikanda ndipo
chakutsogolo kwake kunazikidwa nthenga yanthiwatiwa.
Anavala chijasi cholekeza m’mawondo ndipo chijasicho chinali
chopangidwa ndi chikopa chakambuku. Anali atavala buluku
lansalu yokhuthala kwambiri yoti kuimika pansi ikanatha kuima
yokha. Manja ake anali atawalowetsa m’matumba a chijasicho
mokhala ngati wagwira chinachake.
Guthera komanso Muriuki omwe analinso m’holoyo
anayang’anizana modabwa.
Aliyense anangokhala chete ali dwii kuti aone zomwe
zitachitike. Iwo sankakhulupirira kuti munthu wanzeru zake
angachite za ukadziwotche ngati zimenezo n’kufunsa funso
176