Matigari
“Inde, Boy mukumuona apayu, bambo ake anaphedwa ndi
zigawenga chifukwa choti ankatsatira malamulo. Ndiye
tangoonani pamene mwana wakeyu wafika? Kodi akumatoleza
zakudya m’mabini komanso kumtaya? Mungandivomereze kuti
zimenezo si zimene amachita! Ndi mpondamatiki komanso
munthu wofunika kwambiri m’dziko muno. Komanso tagan-
izirani ineyo. Ndili ndi nyumba yansanjika zisanu ndi ziwiri.
Kunyumba kwanga kuli madamu osambira atatu . . . inde, ata-
tu . . . lina la ana anga, lina la alendo komanso lina la ineyo ndi
mkazi wanga! M’nyumba mwanga mulinso mabafa apamwam-
ba amadzi otentha omwe mapulani ake analembedwa ndi anthu
a ku Finland. Nyumba yanga inakongoletsedwa ndi miyala
yamtengo wapatali ya mabo yochokera ku Italy. Miyala ya k u it-
aly yabwino kwambiri! Ndilinso ndi zinthu zina zomwe angelezi
amazitchula kuti Co at o f Arm s, mwina kwa ena omwe
simukuzidziwa bwinobwino, zimenezi ndi zizindikiro za nyum-
ba yanga komanso banja langa. Chizindikiro chimenechi ndi
chithunzi chamunda wakhofi, ndipo m’mbali mwake muli zik-
wapu ziwiri. Pamunsi pa zimenezi pali mawu athu apamtima:
Kuthana ndi Zigawenga. Imeneyitu ndi mphoto imene anthu omwe
akhala akutsatira malamulo kungochokera m’nthawi ya at-
samunda amapeza. Koma nanga bwanji ana a anthu omwe
anatenga nkhwangwa komanso mifuti yopanga okha n’ku-
manena kuti akulimbana ndi lamulo? Ali kuti lero anthu ame-
newa? Kodi ufulu umene ankamenyerawo uli kuti? N’chifukwa
chaketu amangokhalira kubwebwetuka pansi penipeni pa-
makwerelo a ulemelero.”
“Kunena zoona ndi anthu okhawo omwe ankatsatira mal-
amulo amene anateteza dzikoli kuti lisawonongedwe. Ngati
mutaonetsetsa, osasokonezedwa ndi olemba mabuku ena omwe
162