Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 158

Matigari “Koma mvetserani kaye pang’ono. Ndife odala m’dziko mu- no chifukwa mtsogoleri wathu, Pulezidenti Ole, ndi munthu woopa Mulungu komanso ndi Mkhristu. Ndi munthunso woona patali kwambiri. Iye ali ndi unduna womwe umaona nkhani ya choonadi ndi chilungamo. Nayonso Nduna Yoona Zachilunga- mo, monga amachitira apulezidenti athu, sijomba kutchalitchi. Ndunayi ikubwera kudzayendera anthu a m’dera lino. Monga mukudziwira, amakonda kupita m’madera osiyanasiyana n’kumauza anthu kuti amayesetsa kuonetsetsa kuti chilungamo chikuchitika komanso kuti m’dziko muno muli bata ndi mtende- re. Mwachitsanzo, akhala akuchititsa msonkhano madzulo ano muholo yaikulu ya m’tauni muno. Akufuna kukonza mavuto omwe akuchititsa kuti ogwira ntchito azipanga masitiraka. Pilizi chonde, pitani kwa Nduna Yoona Zachilungamo n’kukaifunsa kuti: Kodi ndi kuti kumene munthu angapeze choonadi ndi chi- lungamo m’dzikoli?” 157