Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Seite 156
Matigari
“Wolima uja anayamba ndi kubwiritsa dothi wantchito wa
munthu amakolola pamene sanalime uja. Kenako anagwetsanso
bwanayu n’kumuponda pachifukwa akuimba nyimbo
yachipambano ndipo anauyamba wobwerera kwawo. Koma
mukudziwa amene anamupeza atafika kunyumba kwake kuja?
Anapezatu mwana wa munthu yemwe amakolola pamene
sanafese uja ali limodzi ndi wantchito wake. Anthu amenewa
ndi amene anaitana apolisi n’kumumangitsa. Munthu wamku-
lu, munthu wanzeru komanso wansembe wathu, kodi
mwanena kuti dzikoli silinasokonekerere? Kodi sitinganene
kuti dzikoli lazondoka tikaona:
Munthu amene akumanga nyumba akugona pamtetete,
Munthu amene akugwira ntchito akuyenda chimanjamanja
Telala akuyenda buno bwamuswe. Komanso wolima akugona
kumimba kukulira malikhweru?”
“Tandiuzeni, kodi choonadi ndi chilungamo chili kuti pame-
nepa? Kodi ndi kuti m’dzikoli kumene ndingakapeze chilunga-
mo?”
Pofika pano, wansembe uja anali atatopa kumvetsera ma-
funso komanso nkhani zitalizitali za Matigari. Nkhawa anali
nayo ija yoti mwina ndi Khristu yemwe wabweranso inali itaba-
lalika. Iye ankaona kuti sizingatheke kuti Ambuye abwere
mwanjira imeneyi n’kumafunsa mafunso opanda nzeruwo ko-
manso kumakamba nthano zokhudza ndale. Kenako anayasam-
ula ngati mvuu pofuna kusonyeza Matigari kuti watopa. Ke-
nako anayang’ana wotchi yake pankono n’kunena kuti:
“Mukudziwa, dzuwa siliima kaye n’kumadikira kuti mfu-
mu idutse. Nthawi sikundidikira, ndili ndi mwambo
wamapemphero woti ndikachititse kwinakwake. Mwandifunsa
mafunso awiri ndipo ndiyesetsa kuti ndiwayankhe.”
155