Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 145

Matigari Gawo 15 Mphunzitsiyo anali kunyumba kwake, cholembera chili m’manja. Atangomuona Matigari, mphamvu zinamuthera. Ana- mulandira Matigari ndi funso. “Kodi mwabwera kudzatani kuno?” “Ndakhala ndikuyendayenda paliponse—” “Kodi simunamve zimene alengeza pawailesi zija?” mphunzitsiyo anamudula mawu Matigari. “Nkhani yotani?” “Akukufunafunanitu paliponse.” “Akufunafuna munthu amene akufufuza choonadi?” “Mwambi ujadi umanena zoona: Nthawi zina munthu wosa- ka amapezeka kuti iyeyo ndi amene akusakidwa. Dzikoli silili mmene linalili kale, kapena mmene linalili pamene tinkamenya nkhondo yomenyera ufulu wathu wodzilamulira. Lero tikungo- khala ngati si ifenso eni ake a dziko lino, moti palibe chilichonse chomwe tingachite momasuka m’dzikoli. Ndikuganiza zosamu- kira dziko lina komwe kulibe mavuto ngati amene ali kunowa.” “Dzikoli lili ndi mbali ziwiri,” anatero Matigari kwa mphunzitsi uja. “Pali mbali ya anthu omwe amangovomereza zinthu mmene zilili, ndiye pali mbali ina ya anthu omwe amafu- na kusintha zinthu. Kodi inuyo muli mbali iti?” “Mwati bwanji? Kusintha zinthu? Mukutanthauza kuyamba kulimbana ndi boma? Kodi nanunso muli m’gulu la anthu om- we akumalimbikitsa ena kuti aukire boma? Ndikuganiza kuti zingakhale bwino kuti muchoke pakhomo panga pano. Sindikufuna kuti maganizo anuwo andilowetse ine m’mavuto. Mtima wofuna kusintha zinthu poukira boma uli ngati matenda a khate . . . ” 144