Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 143
Matigari
chaperekedwa pawailesi lero? Ophunzira asanu a pasukulu ya
ukachenjede agamulidwa kuti akakhale kundende yachitetezo
chokhwima kwa zaka zisanu. Koma si zokhazo . . . ”
Wophunzirayo anayankhula mokayikira. Iye anali wokhu-
mudwa kwambiri. Pamene ankayankhula mawu ake ankamveka
ndi misozi ya zaka zambiri. “Kodi tasiyana liti? Kodi si madzulo
a dzulo laliwisiri? Kapena ndi dzana? Kaya ndiliti kaya. Kaya
ndi dzulo, dzana, kaya chaka chatha, zinthu zakhala zikuchitika
chimodzimodzi. Sizikusinthayi. Ndinathawira kusukulu kuti
ndikabisale pakati pa anzanga. Ndinamva zoti aitanitsa
msonkhano woti apempherere anzawo amene amangidwa.
Amafunanso kuti apempherere mtendere komanso chikondi
m’dziko muno. Oh! Mukudziwa zimene tinakumana nazo ku-
meneko? Tinakumana ndi tsoka lofanana ndi limene ogwira
ntchito pafakitale aja anakumana nalo. Pamene timagwada kuti
tiyambe kugwa nalo pemphero, titatseka m’maso,
tinangozindikira kuti asilikali ndi apolisi atizungulira. Ophunzi-
ra atubulidwa koopsa moti ena awathyola dziboda. Ophunzira
makumi awiri ndi asanu anaphedwa nthawi yomweyo. Mtsi-
kana m’modzi anali woyembekezera ndi mimba ya miyezi isanu
ndi itatu . . . Anamumenya moti wapita padera. Koma ayi ndithu
dzikoli latembenukadi! Kodi zonsezi, zonse zimene zachitikazi
zalengezedwa pawailesi paja, pa Wailesi ya Choonadi yadya
waniyi? Ayi! Zimene alengeza ndi zoti sukulu yaukachenjedeyo
yatsekedwa chifukwa ophunzira anachita sitiraka chifukwa sa-
kupatsidwa chakudya chabwino.”
“Limenelotu ndi bodza lankunkhuniza! Ineyo, ineine, ndinali
komweko! Ndine mboni pankhaniyi. Ndangopulumukira pa-
kangaude n’kuthawa kubwera kuno. Koma ndaphunzirapo zin-
thu zingapo. Pulezidenti Ole sakusewera ndi munthu.
142