Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 134
Matigari
lachenjeza kuti silinyengerera chipembedzo chilichonse chomwe chinga-
pitirize kufalitsa mphekesera yakuti Yesu wabweranso. Lachenjezanso
kuti lilanda malaisesi kwa eni matatu* onse omwe angalole kuti nkhani
zimenezi zizikambidwa m'magalimoto awo. Aliyense ayenera kudziwa
kuti amenewa ndi aneneri onyenga. Sizingatheke kuti Yesu abwere
mādziko muno asanakambirane kaye ndi mtsogoleri wadziko lino,
Pulezidenti Ole. Aliyense akulimbikitsidwa kukanena kupolisi ngati at-
amva munthu wina akunena kuti iyeyo ndi Yesu kapena Gabrieli.
*Matatu: Mawuwa poyamba ankagwiritsidwa ntchito ponena za magalimoto oyenda popan-
da chilolezo. Koma pano amangonena za magalimoto amatola onse komanso
mabasi omwe mumadzadza anthu ndipo nthawi zambiri anthu amakambirana
nkhani zosiyanasiyana zomwe zangochitika kumene kuphatikizaponso mabodza.
Gawo 10
Wofunafuna choonadi ndi chilungamo anataya mtima. Koma
wofufuza chilungamo weniweni satopa ngakhale nsapato zake
zitatha ndi kuyenda. Mlimi sasiya kudzala mbewu kokha chifu-
kwa choti mbewu ina sikumera. Kuti munthu apindule amafu-
nika kukhala wolimbika komanso safunika kutopa ndi kugogo-
da. Choonadi chiyenera kufufuza chilungamo. Chilungamo
chiyenera kufufuza choonadi. Chilungamo chikapambana,
choonadi chimalamulira dziko.
133