Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 132

Matigari Gawo 9 Mutu unali utamukulira. Kenako anapita pakamtini ina yomwe inali pafupi ndi nsewu ndipo anaitanitsa kapu ya nten- thandevu. Anafunsa mwini kamtiniyo kuti, "Kodi ndi kuti kom- we ndingapeze choonadi komanso chilungamo kuno?" Mwini kamtiniyo anamuyang'ana modabwa ngati sanamve funso limene anafunsa. "Ife ochita mabizinezi ang'onoang'ono sitilabada kapena ku- dera nkhawa za nkhani zimenezo. Mukanakhala kuti mwandi- funsa zoti ndi kuti kumene tingapite kuti tikagule shuga wotchi- pa, n'cholinga choti tigulitse n’kupeza kaphindu kochepa, ndi- kanadziwa mmene ndikanakuyankhirani. Koma popeza mwa- funsa nkhani imeneyi, talekani ndikutsegulireni Wailesi ya Choonadi!" . . . zombo zamlengalenga . . . dziko la United States . . . Soviet Un- ion . . . EEC . . . China . . . Japan . . . mabomba a nyukiliya . . . ANC . . . PLO . . . SWAPO . . . Nicaragua . . . El Salvador . . . Mtsogoleri wa dziko lino, Pulezidenti Ole . . . Pulezidenti Ole . . . Mtsogoleri wa dziko lino . . . Anthu ambiri akuyamikira mtsogoleri wathu, Ole . . . Imeneyo inali mitu yathu ya nkhani pano pa Wailesi Yanu ya Choonadi. Tsopano mvetserani nkhanizi mwatsatanetsatane . . . Chidziwitso chapadera . . . Boma lachenjeza kuti aliyense asamale ndi chigawenga china chomwe chikuyendayenda m'dziko muno n'kumauza anthu kuti ndi Matigari ma Njiruungi. Boma lati anthu onse omenyera ufulu wadziko lathu anabwerera kuchoka kunkhalango patsiku limane tinalandira ufulu wathu wodzilamulira. Tonse ndife omenyera ufulu wadziko lino. Anthu amene akufalitsa za munthu ameneyu akusokone- za mtendere mofanana ndi asilikali ananyanyala ntchito aja . . . 131