Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 124
Matigari
Pamenepo, Matirari anaima mbali ina yansewu ndipo ana-
wapatsa azimayiwo malonje:
“Wawatu azimayi! Ndimafuna ndifunse nawo: Kodi ndi kuti
m’dziko muno kumene munthu angapeze choonadi komanso
chilungamo?”
“Kodi bamboyu nayenso akufunsa chiyani? Mwinatu ndi
wogwiririra, odi ndidzipita ine.”
“Inenso ndiuyambe.”
“Basi tionana atsikana . . .”
Onse anasenza mitsuko komanso zidebe zawo n’kubalalika.
Iye analowera chakwinakwake komwe kunali minda . . .
“Kodi ndi zoona kuti John Boy Junior amachita mantha
kwambiri moti mpaka anazikodzera?”
“Anachita zoposa pamenepo!”
“Zoona? Munthu wokhupuka ngati amene uja kufika mpaka
podziipitsira m’kabudula?”
“Nawenso ukanachita zomwezo ukanakhala kuti munthu
wina wakupezeketsa mmene zinalili ndi iyeyo. Kuwonekera
nyangalazi pamaso pa anthu kuti umadzitama komanso kumay-
erekedwa ndi chuma cha eni! Ndiye tangoganiza mmene
ukanamvera mwiniwakeyo akukuuza kuti: ‘Kodi ukuchita chi-
yani ndi katundu wanga?’ Kodi nawenso sukanadziwonongera
m’buluku?”
“Kodi ndi zoona kuti nayenso Robert Williams anali komwe-
ko?
“Inde. Munthu ndi wantchito waketu sasiyana. Matigari ana-
wazindikira mwansanga. Onse anakwera pamahatchi omwe
amathamanga jidimujidimu n’kumalowera kugeti. Koma
123