Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Página 109

Matigari Gawo 1 Ana a kumanda a galimoto aja atangodzuka tsiku lotsatira, anapeza Muriuki akugona mu Mercedes-Benz yake ndipo anamudzutsa n’kukhala momuzungulira. “Kodi wabwera nthawi yanji?” “Usiku?” “Tatiuze . . . tatiuze za Matigari ma Njiruungi.” Mphepo ya nkhani ya mmene Matigari anapulumutsira Guthera inali itawapeza kale. Iwo anamva mmene apolisi anachitira mantha pamene Matigari ankawayankhula. Wap- olisiyo anali yemwe uja ankangokhalira kuwazunza kwa zaka zambiri. Anawa ankadziimba mlandu kwambiri. Iwo ankadzi- funsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani tinagenda munthu wabwino ngati ameneyu? Kodi Muriuki ali kuti atifotokozere za munthu ameneyu?’ N’chifukwa chaketu anadzukirira m’mawa n’kupita kukakumana ndi Muriuki. Naye Muriuki anawonjezera thendo munkhaniyi. Anyama- tawo anagoma zedi ndi zimene anawafotokozera. Iwo ankafun- sa kuti: ‘N’zoona kuti anamangidwa? N’zoona kuti zitseko za ndende zinawatsegukira modabwitsa? Kodi nkhani imeneyi ailengeza pawailesi?’ Nthawi yomweyo mwana wina anathamanga kukatenga wailesi yomwe anaitola kumtaya ija. Anawo anagwirizana kuti wailesiyo ikhala ya mudzi wonse n’cholinga choti azidziwa zomwe zikuchitika m’dziko. Iwo anapereka ndalama ya chipu- kutamisozi kwa mwana amene anatola wailesiyo. Anawa anka- tenga wailesiyi kulikonse komwe ankalowera. Onse anasonkhana malo amodzi mozungulira wailesiyo n’kumamvetsera nkhani. Iwo ankafuna kumva zokhudza 108